PEMPHERO LOKAKAMIZA LALIFUPI (#13438)

Ndichitira umboni, O Mulungu wanga, kuti Munandilenga ine, kuti ndikudziweni ndi kukupembedzani. Nditsimikizira, panthawi ino, kufooka kwanga ndi kukula kwa mphamvu Zanu, kusauka kwanga ndi kulemera Kwanu.  
Kulibe Mulungu wina koma Inu, Wothandiza pa Tsoka, Wodzidalira Nokha.

-Bahá'u'lláh
-----------------------

